Lamentations 2:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta adakhala ngati mdani, adaononga Israele. Adaononga nyumba zonse zachifumu, malinga ao onse adaŵasandutsa mabwinja. Adachulukitsa kulira ndi kudandaula pakati pa anthu a ku Yuda.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Yehova wasanduka mdani, wameza Israele; wameza zinyumba zake zonse, wapasula malinga ake; nachulukitsira mwana wamkazi wa Yuda maliro ndi chibumo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ambuye ali ngati mdani; wawonongeratu Israeli; wawonongeratu nyumba zake zonse zaufumu ndipo wawononga malinga ake. Iye wachulukitsa kubuma ndi kulira kwa mwana wamkazi wa Yuda.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Yehova wasanduka mdani, wameza Israyeli; Wameza zinyumba zace zonse, wapasula malinga ace; Nacurukitsira mwana wamkazi wa Yuda maliro ndi cibumo.