Lamentations 2:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adapasula Nyumba yake ngati khumbi lam'munda, malo ake a msonkhano adaŵasandutsa bwinja. Chauta adathetseratu ku Ziyoni masiku achikondwerero ndi a Sabata. Ndipo atakwiya kwambiri adanyoza mfumu pamodzi ndi ansembe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Wachotsa mwamphamvu dindiro lake ngati la m'munda; waononga mosonkhanira mwake; Yehova waiwalitsa anthu msonkhano ndi Sabata m'Ziyoni; wanyoza mfumu ndi wansembe mokwiya mwaukali.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Wagwetsa malo ake okhalamo ngati khumbi la mʼmunda; wawononga malo ake a msonkhano. Yehova wayiwalitsa Ziyoni maphwando ake oyikika ndi masabata ake. Mokwiya kwambiri, Iye ananyoza mfumu ndi wansembe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Wacotsa mwamphamvu dindiro lace ngati la m'munda; Waononga mosonkhanira mwace; Yehova waiwalitsa anthu msonkhano ndi sabata m'Ziyoni; Wanyoza mfumu ndi wansembe mokwiya mwaukali.