Lamentations 2:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta adanyoza ngakhale guwa lake lomwe, ndipo adaŵakana malo ake opatulika. Adapereka malinga a nyumba zake zachifumu m'manja mwa adani ake. M'nyumba yeniyeni ya Chauta adaniwo adafuula ndi chimwemwe monga momwe zimachitikira pa tsiku lachikondwerero.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ambuye wataya guwa lake la nsembe, malo ake opatulika amnyansira; wapereka m'manja a adani ake makoma a zinyumba zake; iwo anaphokosera m'nyumba ya Yehova ngati tsiku la msonkhano.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ambuye wakana guwa lake la nsembe ndipo wasiya malo ake opatulika. Iye wapereka makoma a nyumba zake zaufumu kwa mdani wake; adaniwo anafuwula mʼnyumba ya Yehova ngati kuti ndi pa tsiku la chikondwerero.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ambuye wataya guwa lace la nsembe, malo ace opatulika amnyansira; Wapereka m'manja a adani ace makoma a zinyumba zace; Iwo anaphokosera m'nyumba ya Yehova ngati tsiku la msonkhano.