Lamentations 2:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta adaatsimikiza zoti aononge malinga a mzinda wa Ziyoni. Adauyesa ndi chingwe chake, ndipo sadafune kuleka kuuwononga kotheratu. Adaliritsa okhala pa malinga ndi pa makoma ake, onsewo akuzunzikira limodzi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Yehova watsimikiza mtima kupasula linga la mwana wamkazi wa Ziyoni; watambalika chingwe, osabweza dzanja lake kuti lisaonongepo; waliritsa tchemba ndi linga; zilefuka pamodzi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova anatsimikiza kugwetsa makoma a mwana wamkazi wa Ziyoni. Anawayesa ndi chingwe ndipo sanafune kuleka kuwagwetsa. Analiritsa malinga ndi makoma; onse anawonongeka pamodzi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Yehova watsimikiza mtima kupasula linga la mwana wamkazi wa Ziyoni; Watambalika cingwe, osabweza dzanja lace kuti lisaonongepo; Waliritsa chemba ndi linga; zilefuka pamodzi.