Lamentations 2:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zipata za mzindawo zakwiririka pansi. Mipiringidzo yake yathyoka ndi kusakazika. Mfumu yake ndi akalonga ake ali ku ukapolo pakati pa anthu akunja, malamulo a Mulungu palibenso oŵalalika. Aneneri ake omwe sakuchitanso zija zoona zinthu m'masomphenya zochokera kwa Mulungu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Zipata zake zalowa pansi; waononga ndi kuthyola mipiringidzo yake; mfumu yake ndi akalonga ake ali pakati pa amitundu akusowa chilamulo; inde, aneneri ake samalandira masomphenya kwa Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zipata za Yerusalemu zalowa pansi; wathyola ndi kuwononga mipiringidzo yake. Mfumu ndi akalonga ake agwidwa ukapolo pakati pa mitundu ya anthu, palibenso lamulo, ndipo aneneri ake sakupeza masomphenya kuchokera kwa Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Zipata zace zalowa pansi; waononga ndi kutyola mipiringidzo yace; Mfumu yace ndi akalonga ace ali pakati pa amitundu akusowa cilamulo; Inde, aneneri ace samalandira masomphenya kwa Yehova.