Lamentations 4:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta adakwiya kwambiri, nagwetsa pansi mkwiyo wake wamotowo. Adayatsa moto ku Ziyoni ndipo motowo udaononga maziko a mzindawo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Yehova wakwaniritsa kuzaza kwake, watsanulira ukali wake; anayatsa moto m'Ziyoni, unanyambita maziko ake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova wakwaniritsa ukali wake; wagwetsa pansi mkwiyo wake woopsa. Ndipo wayatsa moto mʼZiyoni kuti uwononge maziko ake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Yehova wakwaniritsa kuzaza kwace, watsanulira ukali wace; Anayatsa moto m'Ziyoni, unanyambita maziko ace,