Lamentations 4:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ankangoyendayenda m'miseu ngati akhungu, zovala zao zili magazi psu, mwakuti palibe munthu woti nkuzikhudza.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Asochera m'makwalala ngati akhungu, aipsidwa ndi mwazi; anthu sangakhudze zovala zao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsopano akungoyendayenda mʼmisewu ya mu mzinda ngati anthu osaona. Iwo ndi odetsedwa kwambiri ndi magazi palibe yemwe angayerekeze nʼkukhudza komwe chovala chawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Asocera m'makwalala ngati akhungu, aipsidwa ndi mwazi; Anthu sangakhudze zobvala zao.