Lamentations 4:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta mwiniwake ndiye adaŵamwaza, salabadakonso za iwo. Ansembe sadaŵalemekezenso. Akuluakulu sadaŵamvere chifundo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mkwiyo wa Yehova unawalekanitsa, sadzawasamaliranso; iwo sanalemekeze ansembe, sanakomere mtima akulu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova mwini wake wawabalalitsa; Iye sakuwalabadiranso. Ansembe sakulandira ulemu, akuluakulu sakuwachitira chifundo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mkwiyo wa Yehova unawalekanitsa, sadzawasamaliranso; Iwo sanalemekeza ansembe, sanakomera mtima akulu.