Lamentations 4:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu ankangotilondola nthaŵi zonse, kotero kuti sitinkathanso kuyenda m'miseu yathu. Masiku athu ankacheperachepera, imfa yathu idaayandikira, ndithu chimalizo chinali chitafika.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Amalondola mapazi athu, sitingayende m'makwalala athu; chitsiriziro chathu chayandikira, masiku athu akwaniridwa; pakuti chitsiriziro chathu chafikadi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu ankalondola mapazi athu, choncho sitikanayenda mʼmisewu yathu mu mzinda. Chimaliziro chathu chinali pafupi, masiku athu anali owerengeka, chifukwa chimaliziro chathu chinali chitafika.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Amalondola mapazi athu, sitingayende m'makwalala athu; Citsiriziro cathu cayandikira, masiku athu akwaniridwa; pakuti citsiriziro cathu cafikadi.