Lamentations 4:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Onani ana okondedwa a m'Ziyoni amene kale anali ngati golide kwa ife, tsopano akuŵayesa mbiya zadothi zimene woumba amachita kuumba ndi manja ake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ana a Ziyoni a mtengo wapatali, olingana ndi golide woyengetsa, angoyesedwa ngati mbiya zadothi zozipanga manja a woumba.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Haa! Ana a Ziyoni amtengowapatali amene kale anali ngati golide, tsopano ali ngati miphika ya dothi, ntchito ya owumba mbiya!
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ana a Ziyoni a mtengo wapatari, olingana ndi golidi woyengetsa, Angoyesedwa ngati mbiya zadothi zozipanga manja a woumba.