Lamentations 4:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Wodzozedwa wa Chauta uja, amene anali ngati mpweya wotipatsa moyo, adakodwa m'misampha mwao. Iyeyo amene tinkati adzatithandiza ife okhala pakati pa anthu a mitundu ina.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Wodzozedwa wa Yehova, ndiye mpweya wa m'mphuno mwathu, anagwidwa m'maenje ao; amene tinanena kuti, Tidzakhala m'mthunzi mwake pakati pa amitundu,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Wodzozedwa wa Yehova, mpweya wathu wotipatsa moyo, anakodwa mʼmisampha yawo. Tinaganiza kuti tidzakhala pansi pa mthunzi wake pakati pa mitundu ya anthu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Wodzozedwa wa Yehova, ndiye mpweya wa m'mphuno mwathu, anagwidwa m'maenje ao; Amene tinanena kuti, Tidzakhala m'mthunzi mwace pakati pa amitundu,