Lamentations 4:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kondwerani ndipo musangalale, inu anthu a ku Edomu, inu anthu okhala m'dziko la Uzi. Inunso chikho cha mavuto chidzakufikirani pa nthaŵi yanu. Mudzaledzera mpaka kuvula zovala.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
kondwera nusangalale, mwana wamkazi wa Edomu, wokhala m'dziko la Uzi; chikho chidzapita ngakhale mwa iwenso; udzaledzera ndi kuvula zako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kondwera ndi kusangalala, mwana wamkazi wa Edomu. Iwe amene umakhala mʼdziko la Uzi. Koma iwenso chikho chidzakupeza; udzaledzera mpaka kukhala maliseche.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kondwera nusangalale, mwana wamkazi wa Edomu, wokhala m'dzikola Uzi; Cikho cidzapita ngakhale mwa iwenso; udzaledzera ndi kubvulazako.