Lamentations 4:22 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chilango cha machimo anu, inu anthu a ku Ziyoni, chatheratu, Chauta satalikitsa ukapolo wanu. Koma inu anthu a ku Edomu, Chauta adzakulangani chifukwa cha machimo anu. Zolakwa zanu adzaziwulula poyera.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mphulupulu yako yatha, mwana wamkazi wa Ziyoni, Yehova sadzakutenganso ndende; koma adzazonda mphulupulu yako, mwana wa mkazi wa Edomu, nadzavumbulutsa zochimwa zako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwe mwana wamkazi wa Ziyoni, chilango chako chidzatha; Iye sadzatalikitsa nthawi yako ya ukapolo. Koma Yehova adzalanga machimo ako, iwe mwana wamkazi wa Edomu, ndi kuyika poyera mphulupulu zako.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mphulupulu yako yatha, mwana wamkazi wa Ziyoni, Yehova sadzakutenganso ndende; Koma adzazonda mphulupulu yako, mwana wa mkazi wa Edomu, nadzabvumbulutsa zocimwa zako.