Lamentations 4:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chilango cha anthu anga nchachikulu kwambiri kupambana chilango cha anthu a ku Sodomu, amene adalangidwa pa kamphindi chabe, ndipo panalibe wochitapo kanthu kuti aŵathandize.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti mphulupulu ya mwana wamkazi wa anthu a mtundu wanga, ikula koposa tchimo la Sodomu, umene unapasuka m'kamphindi, anthu osauchitira kanthu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kuyipa kwa anthu anga kunali kwakukulu kuposa anthu a ku Sodomu, amene anawonongedwa mʼkamphindi kochepa popanda owathandiza.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti mphulupulu ya mwana wamkazi wa anthu amtundu wanga, ikula koposa cimo la Sodomu, Umene unapasuka m'kamphindi, anthu osaucitira kanthu.