Lamentations 4:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Akalonga ake anali oŵala koposa chisanu chambee, oyera kuposa mkaka. Matupi ao anali ofiira kupambana miyala ya rubi. Anali ndi maonekedwe okongola ngati miyala ya safiro.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Omveka ake anakonzeka koposa chipale chofewa, nayera koposa mkaka, matupi ao anafiira koposa timiyala toti psu; maonekedwe ao ananga a safiro wa mtengo wapatali.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Akalonga ake anali owala koposa chisanu chowundana ndi oyera kuposa mkaka. Matupi awo anali ofiira kuposa miyala ya rubi, maonekedwe awo ngati miyala ya safiro.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Omveka ace anakonzeka koposa cipale cofewa, nayera koposa mkaka, Matupi ao anafiira koposa timiyala toti pyu; maonekedwe ao ananga a safiro wa mtengo wapatari.