Lamentations 4:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma tsopano nkhope zao zasanduka zakuda ngati mwaye. Palibe amene akuŵazindikira m'miseu. Khungu lao lachita makwinyamakwinya, langoti gwa ngati mtengo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Maonekedwe ao ada koposa makala, sazindikirika m'makwalala; khungu lao limamatira pa mafupa ao, lakhwinyata, lasanduka ngati ndodo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma tsopano maonekedwe awo ndi akuda kuposa mwaye; palibe angawazindikire mʼmisewu ya mu mzinda. Khungu lawo lachita makwinyamakwinya pa mafupa awo; lawuma gwaa ngati nkhuni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Maonekedwe ao ada koposa makala, sazindikirika m'makwalala; Khungu lao limamatira pa mafupa ao, lakhwinyata, lasanduka ngati ndodo.