Lamentations 4:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Amene adaphedwa pa nkhondo anali amwai kwambiri kupambana amene adafa ndi njala. Ameneŵa ankafooka pang'onopang'ono mpaka kutsirizika, chifukwa chosoŵa chakudya.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ophedwa ndi lupanga amva bwino kupambana ophedwa ndi njala; pakuti amenewa angokwalika napyozedwa, posowa zipatso za m'munda.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Amene anaphedwa ndi lupanga aliko bwino kuposa amene anafa ndi njala; chifukwa chosowa chakudya cha mʼmunda iwowa ankafowoka ndi njala mpaka kufa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ophedwa ndi lupanga amva bwino kupambana ophedwa ndi njala; Pakuti amenewa angokwalika napyozedwa, posowa zipatso za m'munda.