Leviticus 1:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake ataidula nthulinthuli nyamayo, atengenso mutu ndi mafuta omwe, ndipo aike zonsezo pa nkhuni zimene zili pa guwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo aikadzule ziwalo zake, pamodzi ndi mutu wake ndi mafuta ake; ndi wansembeyo akonze izi pa nkhuni zili pa moto wa pa guwa la nsembe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka ayidule nyamayo nthulinthuli, ndipo wansembe ayike nthulizo pa guwa, atengenso mutu ndi mafuta omwe, ndipo ayike zonsezi pa nkhuni zimene zikuyaka pa guwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo aikadzule ziwalo zace, pamodzi ndi mutu wace ndi mafuta ace; ndi wansembeyo akonze izi pa nkhuni ziri pa mota wa pa guwa la nsembe.