Leviticus 1:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Wansembe abwere nayo ku guwa, aidule mutu moipotola, ndi kutentha mutuwo paguwapo. Magazi ake aŵathire pansi kuti ayenderere pambali pa guwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo wansembe abwere nacho ku guwa la nsembe, namwetule mutu wake, naitenthe pa guwa la nsembe; ndi mwazi wake aukamulire pa mbali ya guwa la nsembe,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Wansembe abwere nayo ku guwa, ayidule mutu moyipotola ndi kutentha mutuwo pa guwa. Magazi ake awathire pansi kuti ayenderere pambali pa guwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo wansembe abwere naco ku guwa la nsembe, namwetule mutu wace, naitenthe pa guwa la nsembe; ndi mwazi wace aukamulire pa mbali ya guwa la nsembe,