Leviticus 1:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake aing'ambe pakati, phiko lina uku, lina uku, koma osachotsa mapikowo. Kenaka aitenthe pa moto wankhuni wapaguwa. Imeneyo ndiyo nsembe yopsereza, yotentha pa moto, ya fungo lokomera Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
nang'ambe mapiko ake osawachotsa konse ai; ndipo wansembeyo aitenthe pa guwa la nsembe, pa nkhuni zili pamoto; ndiyo nsembe yopsereza, nsembe yamoto, ya fungo lokoma la kwa Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka ayingʼambe pakati, koma asachotse mapiko. Ndipo wansembe ayiwotche pa nkhuni zimene zikuyaka pa guwa. Imeneyi ndi nsembe yopsereza, yowotcha pa moto ndiponso ya fungo lokomera Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
nang'ambe mapiko ace osawacotsa konse ai; ndipo wansembeyo aitenthe pa guwa la nsembe, pa nkhuni ziri pamoto; ndiyo nsembe yopsereza, nsembe yamoto, ya pfungo lokoma la kwa Yehova.