Leviticus 1:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma atsuke matumbo ake pamodzi ndi miyendo yake yomwe. Tsono wansembe aipsereze nyama yathunthuyo pa guwa, kuti ikhale nsembe yopsereza, yotentha pa moto, ya fungo lokomera Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
koma atsuke ndi madzi matumbo ake ndi miyendo yake; ndi wansembe atenthe zonsezi pa guwa la nsembe, zikhale nsembe yopsereza, nsembe yamoto, ya fungo lokoma la kwa Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Munthuyo atsuke zamʼkati mwa nyamayo pamodzi ndi miyendo yake yomwe, ndipo wansembe awotche nyama yonse paguwapo. Iyi ndi nsembe yopsereza, chopereka chowotcha pa moto, cha fungo lokomera Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
koma atsuke ndi madzi matumbo ace ndi miyendo yace; ndi wansembe atenthe zonsezi pa guwa la nsembe, zikhale nsembe yopsereza, nsembe yamoto, ya pfungo lokoma la kwa Yehova.