Leviticus 10:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mose adauza Aroni ndi ana ake otsalira aja, Eleazara ndi Itamara, kuti, “Tengani zopereka za zakudya zimene zatsalako pa nsembe yotentha pa moto ija, yopereka kwa Chauta, ndipo muzidye zosafufumitsa pafupi pa guwa, pakuti zimenezi nzopatulika kopambana.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Mose ananena ndi Aroni, ndi Eleazara ndi Itamara, ana ake otsala, Tengani nsembe yaufa yotsalira ku nsembe zamoto za Yehova, ndi kuidya yopanda chotupitsa pafupi pa guwa la nsembe; pakuti ndiyo yopatulika kwambiri;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mose anawuza Aaroni ndi ana ake otsalawo, Eliezara ndi Itamara kuti, “Tengani zopereka zachakudya zopanda yisiti zimene zatsala pa nsembe zopsereza za kwa Yehova ndipo muzidye pafupi ndi guwa pakuti ndi zopatulika kwambiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Mose ananena ndi Aroni, ndi Eleazara ndi Itamara, ana ace otsala, Tengani nsembe yaufa yotsalira ku nsembe zamoto za Yehova, ndi kuidya yopanda cotupitsa pafupi pa guwa la nsembe; pakuti ndiyo yopatulikitsa;