Leviticus 10:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma nganga yopereka moweyula manja ija, pamodzi ndi ntchafu yopereka, muzidyere pa malo aliwonse oyenera pa zachipembedzo, iweyo ndi ana ako aamuna ndi aakazi amene ali nawe. Zimenezi zapatsidwa kwa iwe kuti zikhale zako ndi za ana ako, kuchokera pa nsembe yachiyanjano imene aipereka Aisraele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi nganga yoweyula ndi mwendo wokweza mudyere izi pamalo poyera; iwe ndi ana ako amuna, ndi ana ako akazi omwe, popeza zapatsidwa gawo lako ndi gawo la ana ako amuna, zochokera ku nsembe zoyamika za ana a Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma iwe pamodzi ndi ana ako aamuna ndi aakazi muzidya chidale chimene chinaweyulidwa ndi ntchafu zimene zinaperekedwa nsembe. Muzidye pamalo woyeretsedwa. Zimenezi zaperekedwa kwa iwe ndi ana ako monga gawo lanu pa zopereka zachiyanjano zimene apereka Aisraeli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi nganga yoweyula ndi mwendo wokweza mudyere izi pamalo poyera; iwe ndi ana ako amuna, ndi ana ako akazi omwe, popeza zapatsidwa gawo lako ndi gawo la ana ako amuna, zocokera ku nsembe zoyamika za ana a Israyeli.