Leviticus 10:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ntchafu yoperekayo ndi nganga yoweyulayo, abwere nazo pamodzi ndi zopereka za nsembe yamafuta yotentha pa moto, ndipo uziweyule, kuti zikhale chopereka choweyula pamaso pa Chauta. Zimenezi zikhale zako ndi za ana ako aamuna uli nawoŵa mpaka muyaya, monga momwe Chauta adaalamulira.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mwendo wokweza, ndi nganga yoweyula adze nao pamodzi ndi nsembe zamoto zamafuta, aziweyule nsembe yoweyula pamaso pa Yehova; ndipo zikhale zako ndi za ana ako amuna, mwa lemba losatha; monga Yehova anauza.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ntchafu imene inaperekedwayo ndi chidale chomwe chinaweyulidwacho abwere nazo pamodzi ndi nsembe ya mafuta ya Yehova yotentha pa moto, ndipo uziweyule kuti zikhale zopereka zoweyula pamaso pa Yehova. Zimenezi zizikhala zako ndi ana ako nthawi zonse monga walamulira Yehova.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mwendo wokweza, ndi nganga yoweyula adze nazo pamodzi ndi nsembe zamoto zamafuta, aziweyule nsembe yoweyula pamaso pa Yehova; ndipo zikhale zako ndi za ana ako amuna, mwa lemba losatha; monga Yehova anauza.