Leviticus 10:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo Aroni adauza Mose kuti, “Taonani, lero anthu apereka nsembe yao yopepesera machimo ndi nsembe yao yopsereza pamaso pa Chauta. Komabe zinthu zoopsa zoterezi zandigwera ine. Nanga ndikadadya zopereka za nsembe yopepesera machimo lero, kodi Chauta akadakondwa?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Aroni analankhula ndi Mose, nati, Taonani, lero abwera nayo nsembe yao yauchimo ndi nsembe yao yopsereza pamaso pa Yehova; ndipo zandigwera zotere; ndikadadya nsembe yauchimo lero, kukadakomera kodi pamaso pa Yehova?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Aaroni anamuyankha Mose kuti, “Lero anthu apereka nsembe yawo yopepesera machimo ndiponso nsembe yawo yopsereza pamaso pa Yehova komabe zinthu zoterezi zandichitikira. Kodi Yehova akanakondwa ndikanadya nsembe yopepesera machimo lero?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Aroni analankhula ndi Mose, nati, Taonani, lero abwera nayo nsembe yao yaucimo ndi nsembe yao yopsereza pamaso pa Yehova; ndipo zandigwera zotere; ndikadadya nsembe yaucimo lero, kukadakomera kodi pamaso pa Yehova?