Leviticus 10:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo Mose adauza Aroni kuti, “Pajatu Chauta adanena kuti, ‘Ndidzaonetsa ulemerero wanga kwa onse amene ali pafupi ndi Ine, ndipo ndidzalemekezedwa pamaso pa anthu onse.’ ” Koma Aroni adakhala chete osalankhula.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Mose anati kwa Aroni, Ichi ndi chimene Yehova ananena, ndi kuti, Mwa iwo akundiyandikiza ndipatulidwa Ine, ndi pamaso pa anthu onse ndilemekezedwa. Ndipo Aroni anakhala chete.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamenepo Mose anawuza Aaroni kuti, “Pajatu Yehova ananena kuti, “ ‘Kwa iwo amene amandiyandikira ndidzaonetsa ulemerero wanga; pamaso pa anthu onse ndidzalemekezedwa.’ ” Aaroni anakhala chete wosayankhula.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Mose anati kwa Aroni, Ici ndi cimene Yehova ananena, ndi kuti, Mwa iwo akundiyandikiza ndipatulidwa Ine, ndi pamaso pa anthu onse ndilemekezedwa. Ndipo Aroni anakhala cete.