Leviticus 10:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mose adaitana Misaele ndi Elizafani, ana a Uziyele, bambo wamng'ono wa Aroni, naŵauza kuti, “Senderani pafupi, achotseni abale anuŵa pa malo oyera ndipo muŵatulutsire kunja kwa mahema.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Mose anaitana Misaele ndi Elizafani, ana a Uziyele, mbale wa atate wa Aroni, nanena nao, Senderani pafupi, nyamulani abale anu muwachotse pakhomo pa malo opatulika kunka nao kunja kwa chigono.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mose anayitana Misaeli ndi Elizafani, ana a Uzieli, abambo angʼono a Aaroni, ndipo anawawuza kuti, “Bwerani kuno mudzachotse abale anuwa pa malo wopatulika ndi kuwatulutsira kunja kwa msasa.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Mose anaitana Misayeli ndi Elizafana, ana a Uziyeli, mbale wa atate wa Aroni, nanena nao, Senderani pafupi, nyamulani abale anu muwacotse pakhomo pa malo opatulika kumka nao kunja kwa cigono.