Leviticus 10:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Mose adauza Aroni ndi ana ake Eleazara ndi Itamara kuti, “Musalilekerere tsitsi lanu, ndipo musang'ambe zovala zanu, kuti mungafe, ndiponso kuti mkwiyo ungagwere mpingo wonse. Koma abale anu a m'fuko lonse la Israele ndiwo alire chifukwa cha imfa ya moto umene Chauta watentha nawo anzanu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Mose anati kwa Aroni, ndi kwa Eleazara ndi Itamara ana ake, Musawinda tsitsi, musang'amba zovala zanu; kuti mungafe, ndi kuti angakwiye Iye ndi khamu lonse; koma abale anu, mbumba yonse ya Israele, alire chifukwa cha motowu Yehova anauyatsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Mose anawuza Aaroni ndi ana ake Eliezara ndi Itamara kuti, “Musalileke tsitsi lanu nyankhalala ndipo musangʼambe zovala zanu kuti mungafe, ndi mkwiyo wa Yehova ungagwere anthu onsewa. Koma abale anu okha, kutanthauza fuko lonse la Israeli ndiwo ayenera kulira omwalira aja amene Yehova wawapsereza ndi moto.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Mose anati kwa Aroni, ndi kwa Eleazara ndi ltamara ana ace, Musawinda tsitsi, musang'amba zobvala zanu; kuti mungafe, ndi kuti angakwiye iye ndi khamu lonse; koma abale anu, mbumba yonse ya Israyeli, alire cifukwa ca motowu Yehova anauyatsa.