Leviticus 11:32 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo nyama zimenezi zikagwera pa chinthu chilichonse zitafa, chinthucho chidzakhala chonyansa, chingakhale chamtengo, kapena chovala, kapena chikopa, kapena chiguduli, kapena chipangizo chilichonse chogwiritsa ntchito iliyonse. Chinthucho achiviike m'madzi, koma chidzakhalabe chonyansa mpaka madzulo. Pambuyo pake chidzakhala chabwino.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo chilichonse chakufa cha izi chikagwera kanthu, kanthuka kadzakhala kodetsedwa; ngakhale chipangizo chamtengo, kapena chovala, kapena chikopa kapena thumba, chipangizo chilichonse chimene agwira nacho ntchito, achiviike m'madzi, ndipo chidzakhala chodetsedwa kufikira madzulo; pamenepo chidzakhala choyera.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iliyonse mwa nyama zimenezi ikafa ndi kugwera pa chiwiya chilichonse, kaya chimagwira ntchito yotani, kaya ndi chopangidwa ndi mtengo, kaya ndi cha nsalu, kaya ndi cha chikopa kapena chiguduli chiwiyacho chidzakhala chodetsedwa. Muchiviyike mʼmadzi chiwiyacho komabe chidzakhala chodetsedwa mpaka madzulo, ndipo kenaka chidzakhala choyeretsedwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ciri conse cakufa ca izi cikagwera kanthu, kanthuka kadzakhala kodetsedwa; ngakhale cipangizo camtengo, kapena cobvala, kapena cikopa kapena thumba, cipangizo ciri conse cimene agwira naco nchito, acibviike m'madzi, ndipo cidzakhala codetsedwa kufikira madzulo; pamenepo cidzakhala coyera.