Leviticus 11:35 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chiwalo chilichonse cha nyama yakufa chikagwera pa chinthu chilichonse, chinthucho chidzakhala chonyansa, kaya ndi uvuni kapena chitofu, zonsezo aziphwanye, poti nzonyansa zimenezo, ndipo zidzakhala zonyansa kwa inu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kanthu ka mtembo wake kakagwa pa zinthu zilizonse zidzakhala zodetsedwa; ngakhale mchembo kapena mphika wovundikika, aziswe; zodetsa izi, muziyese zodetsedwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chiwalo chilichonse cha nyama yakufa chikagwera pa chinthu chilichonse kaya pa uvuni, kapena pa mʼphika, ndiye kuti zinthuzo zidzakhala zodetsedwa, ndipo ziphwanyidwe popeza ndi zodetsedwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kanthu ka mtembo wace kakagwa pa zinthu ziri zonse zidzakhala zodetsedwa; ngakhale mcembo kapena mphika wobvundikika, aziswe; zodetsa izi, muziyese zodetsedwa.