Leviticus 11:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma pakuti pa nyama zobzikula kapena za ziboda zogaŵikanazo, asadye izi: ngamira: imeneyi njonyansa kwa inu pa zachipembedzo, chifukwa ngakhale imabzikula, ziboda zake nzosagaŵikana.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma izi zokha simuyenera kuzidya mwa zobzikulazo, kapena zogawanika chiboda; ngamira, angakhale abzikula, koma yosagawanika chiboda, muziiyesa yodetsedwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“ ‘Koma pali nyama zina zimene zimabzikula kokha kapena ndi zogawikana zipondero zimene simukuyenera kudya. Nyama zimenezi ndi ngamira, ngakhale imabzikula ilibe zipondero zogawikana. Choncho ndi yodetsedwa, musadye.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma izi zokha simuyenera kuzidya mwa zobzikulazo, kapena zogawanika ciboda; ngamila, angakhale abzikula, koma yosagawanika ciboda, muziiyesa yodetsedwa.