Leviticus 11:45 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pakuti Ine ndine Chauta, amene ndidakutulutsani ku dziko la Ejipito kuti ndikhale Mulungu wanu. Tsono mukhale oyera, pakuti Ine ndine woyera.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti Ine ndine Yehova amene ndinakukwezani kukutulutsani m'dziko la Ejipito, ndikhale Mulungu wanu; chifukwa chake mukhale oyera, popeza Ine ndine woyera.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ine ndine Yehova amene ndinakutulutsani ku Igupto kuti ndikhale Mulungu wanu. Tsono mukhale woyera, chifukwa Ine ndine woyera.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti Ine ndine Yehova amene ndinakukwezani kukuturutsani m'dziko la Aigupto, ndikhale Mulungu wanu; cifukwa cace mukhale oyera, popeza ine ndine woyera.