Leviticus 12:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Uza Aisraele kuti mkazi akakhala ndi pakati, nabala mwana wamwamuna, adzakhala woipitsidwa masiku asanu ndi aŵiri, monga pa nthaŵi yake yakusamba.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nena ndi ana a Israele, ndi kuti, Akaima mkazi, nakabala mwana wamwamuna, adzakhala wodetsedwa masiku asanu ndi awiri; monga masiku ake akukhala padera, podwala iye, adzakhala wodetsedwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Awuze Aisraeli kuti, ‘Mkazi akakhala woyembekezera, nabala mwana wa mwamuna, mkaziyo adzakhala wodetsedwa kwa masiku asanu ndi awiri, ngati pa masiku ake akusamba.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nena ndi ana a Israyeli, ndi kuti, Akaima mkazi, nakabala mwana wamwamuna, adzakhala wodetsedwa masiku asanu ndi awiri; monga masiku ace akukhala padera, podwala iye, adzakhalawodetsedwa.