Leviticus 12:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mkaziyo adikirebe masiku ena 33, kuti ayeretsedwe ku matenda ake. Asakhudze kanthu kopatulika kalikonse, ndipo asaloŵe m'malo oyera, mpaka masiku akudziyeretsa atatha.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo akhale m'mwazi wa kumyeretsa kwake masiku makumi atatu kudza atatu; asakhudze kanthu kopatulika, kapena kulowa m'malo opatulika, kufikira adakwanira masiku a kumyeretsa kwake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mkaziyo adikire masiku ena 33 kuti ayeretsedwe ku matenda ake. Asakhudze kanthu kalikonse koyera kapena kulowa mʼmalo wopatulika mpaka masiku a kuyeretsedwa kwake atatha.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo akhale m'mwazi wa kumyeretsa kwace masiku makumi atatu kudza atatu; asakhudze kanthu kopatulika, kapena kulowa m'malo opatulika, kufikira adakwanira masiku a kumyeretsa kwace.