Leviticus 12:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma akabala mwana wamkazi, adzakhala woipitsidwa masabata aŵiri monga pa nthaŵi yake yakusamba. Ndipo mkaziyo adikirebe masiku ena 66, kuti ayeretsedwe ku matenda ake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma akabala mwana wamkazi, akhale wodetsedwa masabata awiri, monga umo amakhala padera; ndipo adzakhala m'mwazi wa kumyeretsa kwake masiku makumi asanu ndi limodzi kudza asanu ndi limodzi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngati abala mwana wamkazi, adzakhala wodetsedwa kwa masabata awiri, monga zikhalira pa nthawi yake yosamba. Ndipo mkaziyo adikire masiku ena 66, kuti ayeretsedwe ku matenda akewo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma akabala mwana wamkazi, akhale wodetsedwa masabata awiri, monga umo amakhala padera; ndipo adzakhala m'mwazi wa kumyeretsa kwace masiku makumi asanu ndi limodzi kudza asanu ndi limodzi.