Leviticus 12:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Tsono masiku akudziyeretsa kwake aja atatha, kapena ndi a mwana wamwamuna kapena a mwana wamkazi, abwere kwa wansembe ndi mwanawankhosa wa chaka chimodzi pa khomo la chihema chamsonkhano, kuti nkhosayo ikhale nsembe yopsereza. Abwerenso ndi bunda la nkhunda kapena njiŵa, kuti aperekere nsembe yopepesera machimo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo atakwanira masiku a kumyeretsa kwake pa mwana wamwamuna, kapena mwana wamkazi, adze naye mwanawankhosa wa chaka chimodzi ikhale nsembe yopsereza, ndi bunda, kapena njiwa zikhale nsembe yauchimo, ku khomo la chihema chokomanako, kwa wansembe;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“ ‘Masiku ake wodziyeretsa akatha, kaya ndi a mwana wamwamuna kapena a mwana wamkazi, abwere kwa wansembe ndi mwana wankhosa wa chaka chimodzi pa khomo la tenti ya msonkhano kuti ikhale nsembe yopsereza. Abwerenso ndi chiwunda cha nkhunda kapena njiwa kuti ikhale nsembe yopepesera machimo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo atakwanira masiku a kumyeretsa kwace pa mwana wamwamuna, kapena mwana wamkazi, adze naye mwana wa nkhosa wa caka cimodzi ikhale nsembe yopsereza, ndi bunda, kapena njiwa zikhale nsembe yaucimo, ku khomo la cihema cokomanako, kwa wansembe;