Leviticus 12:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma ngati alibe mwanawankhosa, atenge njiŵa ziŵiri kapena maundaankhunda aŵiri, imodzi ikhale ya nsembe yopsereza, ndipo inayo ikhale ya nsembe yopepesera machimo. Tsono wansembe achite mwambo wopepesera, ndipo mkaziyo adzakhala woyeretsedwa.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ichi ndi chilamulo cha kwa iye wakubala, kapena mwana wamwamuna kapena wamkazi. Ndipo chuma chake chikapanda kufikira nkhosa, atenge njiwa ziwiri kapena maunda awiri; lina likhale nsembe yopsereza, ndi lina nsembe yauchimo; ndi wansembe amchitire chomtetezera, ndipo adzakhala woyera.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngati mkaziyo sangathe kupeza mwana wankhosa, abwere ndi njiwa ziwiri kapena mawunda ankhunda awiri: imodzi ikhale ya nsembe yopsereza ndipo inayo ikhale ya nsembe yopepesera machimo. Tsono wansembe achite mwambo wopepesera wa mkaziyo ndipo adzayeretsedwa.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ici ndi cilamulo ca kwa iye wakubala, kapena mwana wamwamuna kapena wamkazi. Ndipo cuma cace cikapanda kufikira nkhosa, atenge njiwa ziwiri kapena maunda awiri; lina likhale nsembe yopsereza, ndi lina nsembe yaucimo; ndi wansembe amcitire comtetezera, ndipo adzakhalawoyera.