Leviticus 13:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Khatelo likafalikira pa khungu, kotero kuti likhala litagwira khungu lonse la munthu wodwalayo kuyambira kumutu mpaka kumapazi, monga m'mene wansembe angaonere,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ngati khate libukabuka pakhungu, ndi khate lakuta khungu lonse la wanthendayo kuyambira mutu wake kufikira mapazi ake, monga momwe apenyera wansembe;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ndipo ngati, mʼkuona kwa wansembe, khate lija lafalikira pa khungu lonse moti lamugwira thupi lonse kuyambira kumutu mpaka kumapazi,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ngati khate libukabuka pakhungu, ndi khate lakuta khungu lonse la wanthendayo kuyambira mutu wace kufikira mapazi ace, monga momwe apenyera wansembe;