Leviticus 13:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Munthu akakhala ndi chithupsa pathupi pake, kapena m'buko, kapena chikanga, ndipo mwina nkusanduka ngati nthenda ya khate pakhungu pakepo, munthuyo abwere naye kwa wansembe Aroni kapena kwa aliyense mwa ana ake amene ali ansembe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ngati munthu ali nacho chotupa, kapena nkhanambo, kapena chikanga pa khungu la thupi lake, ndipo isandulika nthenda yakhate pa khungu la thupi lake, azifika kwa Aroni wansembe, kapena kwa mmodzi wa ana ake ansembe;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Munthu akakhala ndi chithupsa, kapena mʼbuko, kapena chikanga pa thupi lake chimene chitha kusanduka nthenda ya khate, abwere naye munthuyo kwa Aaroni wansembe kapena kwa mmodzi mwa ana ake amene ndi ansembe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ngati munthu ali naco cotupa, kapena nkhanambo, kapena cikanga pa khungu la thupi lace, ndipo isandulika nthenda yakhate pa khungu la thupi lace, azifika kwa Aroni wansembe, kapena kwa mmodzi wa ana ace ansembe;