Leviticus 13:25 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
wansembe aliwonetsetse. Ubweya wapabangapo ukasanduka woyera, ndipo balalo likaoneka kuti lazama, limenelo ndi khate lomwe laphulika pa balalo. Wansembe atchule wodwalayo kuti ndi woipitsidwa. Imeneyo ndi nthenda ya khate.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
pamenepo wansembe achione; ndipo taonani, ngati tsitsi la chikanga lasanduka lotuwa, ndipo chioneka chakumba kubzola khungu; pamenepo ndilo khate lobuka m'kupsamo; ndipo wansembe azimutcha wodetsedwa ndi nthenda yakhate.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
wansembe aonetsetse bangalo, ndipo ngati ubweya wa pa bangapo usanduka woyera, ndipo balalo lioneka kuti ndi lozama, limenelo ndi khate lomwe latuluka pa balalo. Wansembe alengeze kuti munthuyo ndi wodetsedwa. Limenelo ndi khate la pa khungu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
pamenepo wansembe acione; ndipo taonani, ngati tsitsi la cikanga lasanduka lotuwa, ndipo cioneka cakumba kubzola khungu; pamenepo ndilo khate lobuka m'kupsyamo; ndipo wansembe azimucha wodetsedwa ndi nthenda yakhate.