Leviticus 13:28 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma bangalo likakhala pa malo amodzi losafalikira pa khungu, ndipo likuzimirira, limenelo ndi thuza la balalo. Wansembeyo amtchule wodwalayo kuti ndi wosaipitsidwa, popeza kuti nchipsera cha bala lamoto chabe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ngati chikanga chiima pomwepo, chosakula pakhungu koma chazimba; ndicho chotupa chakupsa; ndipo wansembe amutche woyera; pakuti ndicho chipsera chakupsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma ngati bangalo likhala pa malo amodzi wosafalikira pa khungu, ndipo lazimirira, limenelo ndi thuza la bala lamoto, ndipo wansembe alengeze kuti munthuyo ndi woyera. Chimenecho ndi chipsera chamoto.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ngati cikanga ciima pomwepo, cosakula pakhungu koma cazimba; ndico cotupa ca kupsya; ndipo wansembe amuche woyera; pakuti ndico cipsera ca kupsya.