Leviticus 13:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Wansembe aonetsetse pakhungu pali nthendapo. Akapeza kuti ubweya wa pamalo pali nthendapo wasanduka woyera, ndipo kuti nthendayo yazama ndithu kupitirira khungu, ndiye kuti limenelo ndi khate. Wansembe atamuwonetsetsa ndithu, amutchule kuti ndi woipitsidwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo wansembe aione nthenda pa khungu la thupi; ndipo ngati tsitsi la panthenda lasanduka la mbu, ndi nthenda ikaoneka yapitirira khungu la thupi lake, ndiyo nthenda yakhate; ndipo wansembe amuone, namutche wodetsedwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono wansembe ayangʼanitsitse nthendayo pa khungupo, ndipo ngati ubweya wa pamalo pamene pali nthendapo wasanduka woyera, komanso kuti nthendayo yazama mʼkati kupitirira khungu, ndiye kuti nthendayo ndi khate. Wansembe akamuonetsetsa alengeze kuti ndi wodetsedwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo wansembe aione nthenda pa khungu la thupi; ndipo ngati tsitsi la panthenda lasanduka la mbu, ndi nthenda ikaoneka yapitirira khungu la thupi lace, ndiyo nthenda yakhate; ndipo wansembe amuone, namuche wodetsedwa.