Leviticus 13:30 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
wansembe aiwonetsetse nthendayo. Ikaoneka kuti ikuzama, ndipo ubweya ukakhala wachikasu ndi wotetemera, wansembeyo amutchule wodwalayo kuti ndi woipitsidwa. Imeneyo ndi mfundu yonyerenyesa, khate lakumutu kapenanso lakundevu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
wansembe aziona nthenda; ndipo taonani, ngati ioneka yokumba kubzola khungu, ndipo pali tsitsi loyezuka lotetemera; pamenepo wansembe amutche wodetsedwa; ndiyo mfundu, ndilo khate la mutu kapena ndevu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
wansembe aonetsetse balalo ndipo likaoneka kuti lazama, ndipo ubweya wa pamalopo wasanduka wachikasu ndi wonyololoka, wansembe alengeze kuti munthuyo ndi wodetsedwa. Zimenezo ndi mfundu zonyerenyetsa, khate lakumutu kapena ku chibwano.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
wansembe aziona nthenda; ndipo taonani, ngati ioneka yokumba kubzola khungu, ndipo pali tsitsi loyezuka lotetemera; pamenepo wansembe amuche wodetsedwa; ndiyo mfundu, ndilo khate la mutu kapena ndebvu.