Leviticus 13:34 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri, wansembe aiwonetsetsenso mfunduyo, ndipo ikakhala yakuti sidafalikire pa khungu, ndiponso ikaoneka kuti sidazame, wansembe atchule wodwalayo kuti ndi wosaipitsidwa. Tsono wadwalayo achape zovala zake, ndipo akhale wosaipitsidwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo tsiku lachisanu ndi chiwiri aone mfunduyo; ndipo taonani, ngati mfundu njosakula pakhungu, ndipo ioneka yosakula kubzola khungu, wansembe amutche woyera, ndipo iye atsuke zovala zake, nakhala woyera.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa tsiku lachisanu ndi chiwiri wansembe aonetsetsenso mfundu zonyerenyetsazo ndipo ngati sizinafalikire pa khungu ndi kuti sizinazame, wansembe alengeze kuti munthuyo ndi woyera. Tsono achape zovala zake, ndipo adzakhala woyera.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo tsiku lacisanu ndi ciwiri aone mfunduyo; ndipo taonani, ngati mfundu njosakula pakhungu, ndipo ioneka yosakula kubzola khungu, wansembe amuche woyera, ndipo iye atsuke zobvala zace, nakhala woyera.