Leviticus 13:37 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma wansembe akaipenyetsetsa mfunduyo napeza kuti pamera ubweya wakuda, ndiye kuti mfunduyo ndi yopola. Tsono wansembe amtchule wodwalayo kuti ndi wosaipitsidwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma monga momwe apenyera iye, ngati mfundu yaima pomwe, ndipo pamera tsitsi lakuda, mfundu yapola, ndiye woyera, ndipo wansembe amutche woyera.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma ngati wansembe waonetsetsa kuti mfunduzo sizinasinthe ndipo ubweya wakuda wamera pa mfundupo, ndiye kuti wodwalayo wachira. Tsono wansembe alengeze kuti munthuyo ndi woyeretsedwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma monga momwe apenyera iye, ngati mfundu yaima pomwe, ndipo pamera tsitsi lakuda, mfundu yapola, ndiye woyera, ndipo wansembe amuche woyera.