Leviticus 13:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma pakhungupo pakamaoneka kuti mpoyera, ndipo nthendayo sidapitirire khungu, ndipo ubweya wapamalopo sudasanduke woyera, wansembeyo amuike padera munthu wodwalayo masiku asanu ndi aŵiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma ngati chikanga chikhala chotuwa pa khungu la thupi lake, ndipo chikaoneka chosapitirira khungu, ndi tsitsi lake losasanduka loyera, pamenepo wansembe ambindikiritse wanthendayo masiku asanu ndi awiri;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngati chikanga cha pa khungulo chikuoneka choyera, ndipo kuya kwake sikukuonekera kuti kwapitirira khungu ndi ubweya wake pamalopo sunasanduke woyera, wansembe amuyike wodwalayo padera kwa masiku asanu ndi awiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma ngati cikanga cikhala cotuwa pa khungu la thupi lace, ndipo cikaoneka cosapitirira khungu, ndi tsitsi lace losasanduka loyera, pamenepo wansembe ambindikiritse wanthendayo masiku asanu ndi awiri;