Leviticus 13:43 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono wansembe amuwonetsetse wodwalayo, ndipo banga lotupalo likakhala loyera mofiirira pa dazi lapankhongolo kapena lapamphumilo, monga m'mene limaonekera khate pa khungu,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo wansembe azimuona, ndipo taonani, ngati chotupa chake cha nthenda chili chotuuluka pa dazi la pa mutu wake, kapena la pamphumi pake, monga maonekedwe a khate pa khungu la thupi;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono wansembe amuonetsetse wodwalayo ndipo ngati chithupsa cha pa dazi lapankhongo kapena pa dazi lapachipumicho ndi choyera mofiirira monga nthenda ya khate imaonekera,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo wansembe azimuona, ndipo taonani, ngati cotupa cace ca nthenda ciri cotuuluka pa dazi la pa mutu wace, kapena la pamphumi pace, monga maonekedwe a khate pa khungu la thupi;