Leviticus 13:49 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
ndipo nguwiyo ikakhala ndi maonekedwe achisipu kapena ofiira pa chovalapo, kapena pa thonje loluka, kapena pa chikopa, kaya pa chinthu chilichonse chopangidwa ndi chikopa, imeneyo ndi nguwi ndithu, ndipo chovalacho achiwonetse kwa wansembe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ngati nthenda ili yobiriwira, kapena yofiira pachovala, kapena pachikopa, kapena pamuyaro, kapena pamtsendero, kapena pa chinthu chilichonse chopangika ndi chikopa, ndiyo nthenda yakhate; aziionetsa kwa wansembe;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
ndipo ngati pamalo pamene pachita nguwiyo pali ndi maonekedwe obiriwira kapena ofiirira imeneyo ndi nguwi yoyipitsa chovala ndipo chovalacho chikaonetsedwe kwa wansembe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ngati nthenda iri yobiriwira, kapena yofiira pacobvala, kapena pacikopa, kapena pamuyaro, kapena pamtsendero, kapena pa cinthu ciri conse copangika ndi cikopa, ndiyo nthenda yakhate; aziionetsa kwa wansembe;