Leviticus 13:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Wansembe amuwonetsetse wodwalayo pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri. Akaiwona nthendayo kuti sidafalikire pa khungu, pamenepo wansembeyo amtsekere munthu uja masiku asanu ndi aŵiri ena.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo wansembe amuonenso tsiku lachisanu ndi chiwiri; ndipo taonani, monga momwe apenyera iye, nthenda yaima, nthenda siinapitirira pakhungu, pamenepo wansembe ambindikiritsenso masiku asanu ndi awiri ena;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa tsiku lachisanu ndi chiwiri wansembe amuonenso bwino wodwalayo. Ndipo ngati waona kuti nthendayo sinasinthe ndipo sinafalikire pa khungu, amuyikenso wodwalayo padera kwa masiku ena asanu ndi awiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo wansembe amuonenso tsiku lacisanu ndi ciwiri; ndipo taonani, monga momwe apenyera iye, nthenda yaima, nthenda siinapitirira pakhungu, pamenepo wansembe ambindikiritsenso masiku asanu ndi awiri ena;