Leviticus 13:51 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri aiwonetsetsenso nguwiyo. Ikakhala itafalikira pa chovalacho, kapena pa chikopa cha ntchito ya mtundu uliwonse, imeneyo ndi nguwi yoopsa. Chovalacho ndi choipitsidwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
naone nthenda tsiku lachisanu ndi chiwiri; ngati nthenda yakula pachovala, ngakhale pamuyaro, kapena pamtsendero, kapena pachikopa, zilizonse zantchito zopangika ndi chikopa; nthendayo ndiyo khate lofukuta; ndicho chodetsedwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa tsiku lachisanu ndi chiwiri ayionetsetsenso nguwiyo ndipo ngati nguwiyo yafalikira pa chovalacho, chathonje kapena chaubweya, kapena pa chikopacho, kaya ndi cha ntchito ya mtundu wanji, imeneyo ndi nguwi yoopsa ndipo chovalacho ndi chodetsedwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
naone nthenda tsiku lacisanu ndi ciwiri; ngati nthenda yakula pacobvala, ngakhale pamuyaro, kapena pamtsendero, kapena pacikopa, ziri zonse zanchito zopangika ndi cikopa; nthendayo ndiyo khate lofukuta; ndico codetsedwa.